Acts 7:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mwakuti adampulumutsa ku masautso ake onse. Adampatsa nzeru ndi kumkometsa pamaso pa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kotero kuti mfumuyo idamuika kuti akhale nduna yaikulu ya dziko la Ejipito, ndiponso woyang'anira banja lake lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.