Acts 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene adaona kuti Mwejipito wina akuzunza mmodzi mwa abale akewo, Moseyo adatchinjiriza Mwisraeleyo, nalipsira Mwejipito uja pakumupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamtchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ataona mmodzi wa iwo akuzunzidwa ndi Mwigupto, anatchinjiriza Mwisraeliyo, namupha Mwiguptoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona wina woti alikumcitira cotpa, iye anamcinjiriza, nambwezera cilango wozunzayo, nakantha M-aigupto.