Acts 7:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake atabwera, adapeza Aisraele aŵiri akumenyana. Adayesa kuŵayanjanitsa pakuŵauza kuti, ‘Anthuni, muli pa chibale, bwanji mukuvutana?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake Mose anaona Aisraeli awiri akukangana. Iye anayesa kuwayanjanitsa ponena kuti, ‘Amuna inu, ndinu abale; chifukwa chiyani mukufuna kupwetekana?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; mucitirana coipa bwanji?