Acts 7:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaona ndithu kuvutika kwa anthu anga amene ali ku Ejipito. Ndamva kudandaula kwao, ndipo ndabwera kudzaŵapulumutsa. Tiye tsopano, ndikutume ku Ejipito.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali m'Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
7 Kuona ndaona coipidwa naco anthu anga ali m'Aigupto, ndipo a amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto