Acts 7:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Moseyo ndi yemwe uja amene Aisraele aja adaamkana nkumanena kuti, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu?’ Yemweyo Mulungu adamtuma kuti akhale mkulu ndi momboli kudzera mwa mngelo uja amene adaamuwonekera pa chitsamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkuru ndi woweruza? ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkuru, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pacitsamba.