Acts 7:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adauza Aroni kuti, ‘Tipangireni milungu kuti izititsogolera, pakuti sitikudziŵa chimene chamgwera Mose uja, amene adatitsogolera potuluka m'dziko la Ejipito.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m'Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati kwa Aaroni, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitsogolera kutuluka mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
11 nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogoleraife; pakuti Mose uja, amene anatiturutsa m'Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.