Acts 7:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono masiku amenewo iwo adapanga fano la mwanawang'ombe. Adapereka nsembe kwa fanoli, nakondwerera ntchito za manja ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 12 anapanga mwana wa ng'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi nchito za manja ao.