Acts 7:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mulungu adaŵafulatira, naŵapereka ku machimo akupembedza nyenyezi, monga akunenera mau olembedwa m'buku la aneneri kuti, “ ‘Inu Aisraele, musayese kuti munkapereka kwa Ine nyama zimene munkapha ndi kuzipereka ngati nsembe pa zaka makumi anai zija m'chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma 13 Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku laaneneri, 14 Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe Zaka makumi anai m'cipululu, nyumba ya Israyeli inu?