Acts 7:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munkanyamula hema la Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene mudaŵapanga kuti muziŵapembedza. Ndidzakuchotsani kukutayani kutali, kupitirira dziko la Babele.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayi, inu mwanyamula tenti ya Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwapembedza. Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
15 Ndipo munatenga cihema ca Moloki, Ndi nyenyezi ya mulungu Refani, Zithunzizo mudazipanga kuzilambira; Ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwace mwa Babulo.