Acts 7:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
21 Thambo la kumwamba ndilo mpando wacifumu wanga, Ndi dziko lapansi copondapo mapazi anga: Mudzandimangira nyumba yotani? ati Ambuye; Kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?