Acts 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu sadampatseko ndi kadera kakang'onong'ono komwe ka dzikoli kuti kakhale kakekake. Koma adamlonjeza kuti adzampatsa dzikoli kuti likhale lakelake ndiponso la zidzukulu zake, ngakhale pa nthaŵi imeneyo nkuti akadalibe mwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo sanampatsa cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.