Acts 7:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Stefano adapitirira nati, “Ha, anthu okanika inu, mitima yanu njachikunja, makutu anu ngogontha. Nthaŵi zonse, monga ankachitira makolo anu, inunso mumakana kumvera Mzimu Woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
22 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.