Acts 7:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adachita chipangano ndi Abrahamu, chimene chizindikiro chake chinali kuumbala. Motero Abrahamu adaumbala mwana wake Isaki, ali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa. Isaki adaumbala Yakobe, ndipo Yakobe adaumbala makolo athu khumi ndi aŵiri aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.