Acts 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo uja ankavomerezana nawo za kupha kumeneku. Tsiku limenelo mpingo wa ku Yerusalemu udayamba kuzunzidwa kwambiri, ndipo onse, kupatula atumwi okha, adabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano. Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Saulo analikubvomerezana nao pa imfa yace. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukuru pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi samariya, koma osati atumwi ai.