Acts 8:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simoni uja nayenso adakhulupirira, ndipo atabatizidwa, ankakhalira limodzi ndi Filipo. Adazizwa pakuwona zizindikiro ndi zozizwitsa zimene zinkachitika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.