Acts 8:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndiye wakusunga cuma cace conse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;