Acts 8:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa: “Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha, ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta. Sadalankhulepo kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegula pakamwa pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo. Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, Ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga, Kotero sanatsegula pakamwa pace: