Acts 8:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adampeputsa, pa mlandu wake sadamchitire chilungamo. Palibe amene adzatha kusimba za zidzukulu zake, pakuti moyo wake wachotsedwa pa dziko lapansi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa; mbadwo wake adzaubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kucepetsedwa kwace ciweruzo cace cinacotsedwa; Mbadwo wace adzaubukitsa ndani? Cifukwa wacotsedwa kudziko moyo wace.