Acts 8:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Filipo adapezeka kuti ali ku Azoto. Adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino m'mizinda yonse, mpaka adakafika ku Kesareya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Filipo anapezedwa ku Azotu; ndipo popitapitaanalalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kaisareya.