Acts 8:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikiro zimene anazichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikilo zimene anazicita.