Acts 8:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mumzindamo munali munthu wina, dzina lake Simoni amene kale ankachita matsenga, namadodometsa anthu onse a ku Samariyako. Iyeyu ankadzimveketsa kuti ndi munthu wamkulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma panali munthu dzina lace Simoni amene adacita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkuru;