Acts 9:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ku Damasikoko kunali wophunzira wina, dzina lake Ananiya. Iyeyu adaaona m'masomphenya Ambuye akumuitana kuti, “Ananiya!” Iye adati, “Ee, Ambuye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!” Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,