Acts 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera