Acts 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika, cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli;