Acts 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kukampempha makalata opita nawo ku nyumba zamapemphero za ku Damasiko. Ankafuna kuti ngati akapezeko ena otsata Njira ya Ambuye, kaya ndi amuna kaya ndi akazi, akaŵamange nkubwera nawo ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.