Acts 9:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma anthu ena adamuuzako za chiwembucho. Anthu achiwembuwo ankadikira pa zipata za linga la mzinda usana ndi usiku kuti amuphe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ciwembu cao cinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;