Acts 9:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mpingo wa ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.