Acts 9:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Yopa kunali kufupi ndi ku Lida, choncho pamene ophunzira adamva kuti Petro ali ku Lida, adatuma anthu aŵiri kuti akamuuze kuti, “Chonde, mubwere kwathu kuno msanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza ku Yopa kunali pafupi ndi Luda; pamene ophunzira anamva kuti Petro anali ku Luda, anatuma anthu awiri kuti akamudandaulire kuti, “Chonde bwerani kuno msanga!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popeza Luda ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musacedwa mudze kwa ife.