Acts 9:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.