Acts 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adadzuka, koma pamene maso ake adaphenyuka, sadathe kupenya kanthu. Tsono anzake aja adamgwira pa dzanja naloŵa naye m'Damasiko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m'Damasiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.