Amos 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzathyola mpiringidzo woteteza mzinda wa Damasiko. Ndidzaonongeratu mfumu yolamulira ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Betedeni. Anthu a ku Siriya adzatengedwa ukapolo kupita nawo ku dziko la Kiri.” Akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzathyola chipata cha Damasiko; ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni. Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'cigwa ca Aveni, ndi iye wogwira ndodo yacifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.