Amos 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo anyoza malamulo a Ine Chauta, ndipo sadatsate malangizo anga. Milungu yabodza imene makolo ao ankaipembedza yaŵasokeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo akana lamulo la Yehova ndipo sanasunge malangizo ake, popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza, milungu imene makolo awo ankayitsatira,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza akaniza cilamulo ca Yehova, osasunga malemba ace; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;