Amos 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu, anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana. Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi, mwakuti amanyoza dzina langa loyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiwo amene aliralira pfumbi lapansi liri pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wace amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;