Amos 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo, pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole. M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nagona pansi pa zopfunda za cikole ku maguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.