Amos 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani mau amene Chauta adalankhula, mau okudzudzulani inu Aisraele, ndiye kuti banja lonse limene Iye adalitulutsa ku dziko la Ejipito. Adanena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israyeli, kulinenera banja lonse ndinalikweza kuliturutsa m'dziko la Aigupto, ndi kuti,