Amos 3:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Sadziŵa kuchita zolungama amene amadzaza malinga ao ndi zinthu zozipeza mwankhondo ndi mwakuba.” Akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwo sadziwa kuchita zolungama, ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.