Amos 3:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Monga mbusa amangotolako miyendo iŵiri kapena nsonga ya khutu la nkhosa yake ikajiwa ndi mkango, ndimo m'mene adzapulumukire Aisraele okhala ku Samariya, ngati zidutswa chabe za bedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi m'Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu, moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli amene amakhala mu Samariya pa msonga za mabedi awo, ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israyeli okhala pansi m'Samariya, m'ngondya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.