Amos 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku limene ndidzalange Israele chifukwa cha zolakwa zake, maguwa a ku Betele ndidzaŵagumula, ndipo nyanga za guwa zidzathyoka nkugwa pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake, ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli; nyanga za guwa zidzathyoka ndipo zidzagwa pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsiku lakumlanga Israyeli cifukwa ca zolakwa zace, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Beteli; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi.