Amos 3:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzagwetseratu nyumba za nthaŵi yachisanu ndi za nthaŵi yamafundi. Nyumba zaminyanga zidzaonongeka, ndithu nyumba zazikulu zidzaphwasuka.” Akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha; nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yacisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuruzo zidzatha, ati Yehova.