Amos 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mbalame nkukatera pa msampha pansi, popanda nyambo yake? Nanga msamphawo kodi nkufwamphuka pansipo, usanakole kanthu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mbalame nʼkutera pa msampha pamene palibe nyambo yake? Kodi msampha umafwamphuka usanakole kanthu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woichera? Kodi msampha ufamphuka pansi wosakola kanthu?