Amos 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ulengeze kwa anthu okhala m'malinga a ku Asidodi, ndiponso kwa okhala m'malinga a ku Ejipito, uŵauze kuti akasonkhane ku mapiri a ku Samariya, akaone zachipwirikiti ndi zachifwamba zimene zikuchitika pakati pa anthu ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto: “Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya; onani chisokonezo pakati pake ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bukitsani ku nyumba zacifumu za Asidodi, ndi ku nyumba zacifumu za m'dziko la Aigupto, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akuru m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwace.