Amos 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mverani mau aŵa akazi inu okhala ku Samariya amene mukungonenepa ngati ng'ombe za m'dera la Basani, inu amene mumavutitsa osauka ndi kuzunza osoŵa. Ntchito nkumangolamula amuna anu kuti, “Tipatseni zoziziritsa kukhosi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya, inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basana, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani naco, timwe.