Amos 4:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidakugwetserani miliri yonga ya ku Ejipito ija. Ndidaphetsa achinyamata anu ku nkhondo, ndidapereka akavalo anu kwa adani. Ndidakununkhitsani fungo la mitembo lochokera ku misasa yanu yankhondo. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndinabweretsa miliri pakati panu monga ndinachitira ku Igupto. Ndinapha anyamata anu ndi lupanga, ndinapereka akavalo anu kwa adani. Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Aigupto; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa cigono canu kufikitsa kumphuno kwanu; ikoma simunabwerera kudzakwa Ine, ati Yehova.