Amos 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono inu Aisraele ndidzakuteroni. Ndipo chifukwa choti ndidzakuchitani zimenezi, inu Aisraele, konzekani kuti mukumane ndi Mulungu wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli, chifukwa ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzatero nawe, Israyeli; popeza ndidzakucitira ici, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israyeli.