Amos 4:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tamvani, Iyeyo ndiye amene amaumba mapiri ndi kupanga mphepo, ndiye amene amaululira munthu za m'maganizo mwake, ndiye amene amasandutsa usana kuti ukhale usiku, ndiye amene amayenda pa zitunda za dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amene amawumba mapiri, amalenga mphepo, ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake, Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima, ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi, dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ace, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova Mulungu wamakamu.