Amos 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndinenso amene ndinamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina, koma pa mzinda wina ayi, mvula inkagwa pa munda wina; koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinabvumbistira mudzi umodzi mvula, osabvumbitsira mudzi wina; munda wina unabvumbidwa mvula, ndi m'munda mosabvumbidwa mvula munafota.