Amos 4:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero midzi iŵiri kapena itatu inkapita ku mudzi umodzi kuti ikamwe madzi, koma osaŵakwanira. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi, koma sanapeze madzi okwanira kumwa. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu ku mudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhuta; koma simunai bwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.