Amos 4:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidaumitsa mbeu zanu ndi matenda ndiponso ndi chinoni. Chidafotetsa mbeu za m'minda yanu yonse ndi yamphesa yomwe. Dzombe lidaononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi, komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa, ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu. Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni; minda yanu yocuruka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi yaazitona, yaonongeka ndi cirimamine; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.