Amos 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumazunza anthu ochita chilungamo, mumalandira ziphuphu ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzocuruka, ndi macimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira cokometsera mlandu, akukankha osowa kucipata.