Amos 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muike mtima pa zabwino osati pa zoipa, kuti mukhalebe ndi moyo. Apo Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakhala nanu monga mwaneneramo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Funani cokoma, si coipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wamakamu adzakhala ndi inu, monga munena.